Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 20:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti mu Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani mu Basani wa fuko la Manase.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti m'Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani m'Basani wa fuko la Manase.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Kuvuma kwa Yordani, m'mapiri aja a kuvuma kwa Yeriko m'chipululu muja, adapatula Bezeri pakati pa mizinda ya fuko la Rubeni. Pakati pa mizinda ya fuko la Gadi ku Giliyadi adapatula Ramoti. Ndipo pakati pa mizinda ya fuko la Manase ku Basani adapatula Golani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Kummawa kwa Yorodani, mʼmapiri a chipululu a kummawa kwa Yeriko, anapatula Bezeri pakati pa dera la fuko la Rubeni. Anapatulanso Ramoti ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi, ndiponso Golani ku Basani mʼdera la fuko la Manase.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 20:8
12 Mawu Ofanana  

Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Ndipo anamuka Yoramu mwana wa Ahabu kukathira nkhondo pa Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndi Aaramu analasa Yoramu.


ndi tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko analandira, motapa pa fuko la Rubeni, Bezeri m'chipululu ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake,


ndi motapa m'fuko la Gadi, Ramoti mu Giliyadi ndi mabusa ake, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake,


mizinda yonse ya kuchidikha, ndi Giliyadi lonse, ndi Basani lonse kufikira ku Saleka ndi Ederei, mizinda ya dziko la Ogi mu Basani.


ndiyo Bezeri, m'chipululu, m'dziko lachidikha, ndiwo wa Arubeni; ndi Ramoti mu Giliyadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, mu Basani, ndiwo wa Amanase.


Ndipo anapatula Kedesi mu Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.


Iyi ndi mizinda yoikidwira ana onse a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao kuti athawireko aliyense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.


Ndipo anapatsa ana a Geresoni, a mabanja a Alevi, motapira pa hafu la fuko la Manase, Golani mu Basani ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo; ndi Beesetera ndi mabusa ake; mizinda iwiri.


Ndipo motapira pa fuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake,


Ndipo motapira m'fuko la Gadi, Ramoti mu Giliyadi ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa