Yoswa 20:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo azikhala m'mzindamo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wake, mpaka atafa mkulu wa ansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzake azibwerera ndi kufika kumzinda kwake, ndi nyumba yake, kumzinda kumene adathawako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wake, mpaka atafa mkulu wa ansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzake azibwerera ndi kufika kumudzi kwake, ndi nyumba yake, kumudzi kumene adathawako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Munthuyo adzakhala mumzindamo mpaka ataweruzidwa pamaso pa anthu onse, ndiponso mpaka mkulu wa ansembe wa nthaŵi imeneyo atafa. Pamenepo munthuyo angathe kubwereranso kwao, kumudzi kumene adachoka mothaŵa kuja.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Munthu wakuphayo adzakhalabe mu mzindawo mpaka atayimbidwa mlandu pamaso pa gulu lonse, ndiponso mpaka atamwalira mkulu wa ansembe amene akutumikira pa nthawiyo. Pamenepo munthuyo atha kubwereranso ku mudzi kwawo kumene anachoka mothawa kuja.” Onani mutuwo |