Yoswa 20:4 - Buku Lopatulika4 Munthu akathawira umodzi wa mizinda iyi, aziima polowera pa chipata cha mzindawo, nafotokozere mlandu wake m'makutu a akulu a mzindawo; pamenepo azimlandira kumzinda kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa chipata cha mudziwo, nafotokozere mlandu wake m'makutu a akulu a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Angathe kuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyo, nakafika pa malo achiweruzo amene ali pa chipata cha mzindawo. Atafika, asimbire atsogoleri mlandu wakewo. Apo atsogoleriwo adzamlola kuloŵa mumzindamo, nadzampatsa malo oti azikhalako. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Ngati munthu wathawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, akafike pa malo oweruzira milandu amene ali pa chipata cha mzindawo ndipo akafotokoze mlandu wake pamaso pa akuluakulu a mzindawo. Kenaka iwo adzamulola kulowa mu mzinda wawo ndi kumupatsa malo woti akhale nawo. Onani mutuwo |