Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 2:9 - Buku Lopatulika

9 nati kwa amunawo, Ndidziwa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, ndi kuti kuopsa kwanu kwatigwera, ndi kuti okhala m'dziko onse asungunuka pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 nati kwa amunawo, Ndidziwa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, ndi kuti kuopsa kwanu kwatigwera, ndi kuti okhala m'dziko onse asungunuka pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 naŵauza kuti, “Ndikudziŵa kuti Chauta wakupatsani dziko lonseli, ndipo tonsefe tikuchita mantha, mitima yathu ili thithithi!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 ndipo anawawuza kuti, “Ine ndikudziwa kuti Yehova wakupatsani dziko lino ndipo tili ndi mantha. Anthu onse a mʼdziko lino ali ndi mantha chifukwa cha inu.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 2:9
39 Mawu Ofanana  

Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera mizinda yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo.


Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wake ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisraele onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi.


Pamenepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lake lonse, nadzaima pamaso pake, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu padziko lonse lapansi, koma kwa Israele ndiko; ndipo tsopano, mulandire chakukuyamikani nacho kwa mnyamata wanu.


Popeza Ambuye adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere.


Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu.


Ndi m'maiko monse, ndi m'mizinda yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lake, Ayuda anali nako kukondwera ndi chimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m'dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.


Koma ndidziwa kuti Mombolo wanga ali ndi moyo, nadzauka potsiriza pafumbi.


Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.


Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.


Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.


Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao.


Angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino;


Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.


Pofika mbiriyo ku Ejipito, iwo adzamva kuwawa kwambiri pa mbiri ya Tiro.


Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.


Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.


Pamenepo Mose anatumiza amithenga ochokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israele, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera;


Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.


Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?


Palibe munthu adzaima pamaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, chifukwa cha inu, monga anenana ndi inu.


Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.


Ndipo anthu onse a padziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.


Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele.


Ndi chikhulupiriro Rahabu wadama uja sanaonongeke pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere.


Ndipo titamva ichi mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m'mwamba umo, ndi padziko lapansi.


Ndipo anati kwa Yoswa, Zoonadi, Yehova wapereka dziko lonse m'manja mwathu; ndiponso nzika zonse zasungunuka pamaso pathu.


Koma asanagone iwo, anawakwerera patsindwi iye,


Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele.


Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m'dzanja lako Yeriko ndi mfumu yake, ndi ngwazi zake.


ndi zonse anachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basani wokhala ku Asitaroti.


Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi.


Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yake, ndi zonse anachita mu Ejipito,


Ndipo mnzake anayankha nati, Ichi si china konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yowasi, munthu wa Israele; Mulungu wapereka Midiyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa