Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 2:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo amunawo anawalondola panjira ya ku Yordani yonka kudooko; ndipo atatuluka akuwalondola, anatseka pachipata.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo amunawo anawalondola pa njira ya ku Yordani yonka kudooko; ndipo atatuluka akuwalondola, anatseka pachipata.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Atangochoka anthu otumidwa ndi mfumuwo kutuluka mumzindamo, chipata chidatsekedwa. Ndipo adapita ku mseu kukaŵafunafuna azondiwo, mpaka adakafika ku dooko la Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Nthumwi za mfumu zija zitatuluka ndipo chipata chinatsekedwa. Nthumwizo zinapita kukawafunafuna azondi aja mpaka ku dooko la Yorodani.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 2:7
6 Mawu Ofanana  

nanena, Nyumba yandende tinapeza chitsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense.


ndipo m'mene akadati atseke pachipata, kutada, anatuluka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza.


Koma adawakweretsa patsindwi, nawabisa ndi mitengo yanthamza yoyanika patsindwi.


Koma asanagone iwo, anawakwerera patsindwi iye,


Ndipo Agiliyadi anatsekereza madooko a Yordani a Efuremu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efuremu, Ndioloke, amuna a Giliyadi anati kwa Iye, Ndiwe Mwefuremu kodi? Akati, Iai;


Ndipo ananena nao, Nditsateni ine, pakuti Yehova wapereka adani anu Amowabu m'manja mwanu. Ndipo anatsika ndi kumtsata, natsekereza Amowabu madooko a Yordani, osalola mmodzi aoloke.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa