Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 2:18 - Buku Lopatulika

18 Taona, tikadzalowa m'dzikomo ife, uzimanga chingwe ichi chofiira pazenera pamene watitsitsira; ndipo udzasonkhanitsa m'nyumbamo atate wako ndi mai wako ndi abale ako ndi a m'nyumba onse a atate wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Taona, tikadzalowa m'dzikomo ife, uzimanga chingwe ichi chofiira pazenera pamene watitsitsira; ndipo udzasonkhanitsa m'nyumbamo atate wako ndi mai wako ndi abale ako ndi a m'nyumba onse a atate wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Mvetsa tsono. Tikadzaloŵa, iweyo udzamange chingwe chofiirachi pawindo pomwe watitulutsirapa. Bambo wako, mai wako, abale ako ndi onse a m'banja la bambo wako, adzakhale m'nyumba mwako muno.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 tikadzalowa mʼdzikoli, iwe udzamangirire kansalu kofiira pa zenera limene unatitulutsira, ndi kusonkhanitsa abambo ako, amayi ako, abale ako ndi banja lako lonse mʼnyumba muno.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 2:18
19 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;


Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno.


pakuti ndidzapirira bwanji pakuchiona choipa chilikudzera a mtundu wanga, kapena ndidzapirira bwanji pakuchiona chionongeko cha fuko langa?


Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.


Milomo yako ikunga mbota yofiira, m'kamwa mwako ndi kukoma: Palitsipa pako pakunga phande la khangaza paseri pa chophimba chako.


pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope;


Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa moto ilikupsererapo ng'ombe yaikazi.


Ndipo ayale pa izi nsalu yofiira, ndi kuliphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.


Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.


Ndipo pakukamba naye, analowa, napeza ambiri atasonkhana;


Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.


amene adzalankhula nawe mau, amene udzapulumutsidwa nao iwe ndi apabanja ako onse.


Ambuye achitire banja la Onesifore chifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawirikawiri, ndipo sanachite manyazi ndi unyolo wanga;


Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,


Nati iye, Momwemo, monga mwa mau anu. Ndipo anawauza amuke, iwo namuka; namanga iye chingwe chofiiracho pazenera.


Pamenepo anyamata ozondawo analowa, natulutsa Rahabi, ndi atate wake ndi mai wake ndi abale ake, ndi onse anali nao; anatulutsanso achibale ake onse; nawaika kunja kwa chigono cha Israele.


Koma Rahabi, mkazi wadamayo ndi banja la atate wake, ndi onse anali nao, Yoswa anawasunga ndi moyo; ndipo anakhala pakati pa Israele mpaka lero lino; chifukwa anabisa mithenga imene Yoswa anaituma kuzonda Yeriko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa