Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 2:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakuchitirani chifundo, kuti inunso mudzachitira chifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa chizindikiro choona,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakuchitirani chifundo, kuti inunso mudzachitira chifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa chizindikiro choona,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsopano mulumbire pamaso pa Chauta kuti mudzasunga zimene mulonjeze, ndipo kuti mudzachitira chifundo banja langa, monga momwe ndakusamalirani inu, ndipo munditsimikizire kwenikweni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Choncho mulumbire pamaso pa Yehova ndi kundipatsa chizindikiro choti mudzachitadi zimene mwalonjeza, kuti monga inu ndakuchitirani chifundo, inunso mudzachitira chifundo a pa banja la abambo anga.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 2:12
24 Mawu Ofanana  

tsopano iwe undilumbirire ine pano pa Mulungu kuti sudzandinyenga ine, kapena mwana wanga, kapena mdzukulu wanga: koma monga ufulu ndakuchitira iwe udzandichitire ine, ndi dziko lomwe wakhalamo, ngati mlendo.


ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.


Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu yake ya Abrahamu Mbuye wake, namlumbirira iye za chinthucho.


Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu:


Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lake, nalimbitsa mtima wake kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele.


pakuti ndidzapirira bwanji pakuchiona choipa chilikudzera a mtundu wanga, kapena ndidzapirira bwanji pakuchiona chionongeko cha fuko langa?


Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.


Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.


Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye chisungire.


opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo;


Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.


Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.


kuti mudzawasunga ndi moyo atate wanga ndi mai wanga, ndi alongo anga ndi abale anga, ndi zonse ali nazo, ndi kupulumutsa miyoyo yathu kuimfa.


Taona, tikadzalowa m'dzikomo ife, uzimanga chingwe ichi chofiira pazenera pamene watitsitsira; ndipo udzasonkhanitsa m'nyumbamo atate wako ndi mai wako ndi abale ako ndi a m'nyumba onse a atate wako.


Ndipo kudzakhala kuti aliyense akadzatuluka pa khomo la nyumba yako kubwalo, imfa imeneyi ndi yake, tilibe kupalamula ife; koma aliyense adzakhala ndi iwe m'nyumba, likamfikira dzanja, imfa imeneyi ndi yathu.


Ndipo Yoswa ananena kwa amuna awiri anazonda dzikowo, Lowani m'nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kutulutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munamlumbirira iye.


Ndipo Yoswa anachitirana nao mtendere napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira.


Ndipo alonda anaona munthu alikutuluka m'mzinda, nanena naye, Utionetsetu polowera m'mzinda, ndipo tidzakuchitira chifundo.


Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m'dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa