Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 2:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo titamva ichi mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m'mwamba umo, ndi padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo titamva ichi mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m'mwamba umo, ndi pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Titangomva zimenezi, tonsefe tidataya mtima, ndipo mantha adatigwira kukuwopani inu. Tikudziŵa kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa kumwamba ndi dziko lonse lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Titamva zimenezi, ife tinataya mtima ndipo aliyense wa ife ali ndi mantha chifukwa cha inu. Tikudziwa kuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 2:11
27 Mawu Ofanana  

kuti anthu onse a padziko lapansi akadziwe kuti Yehova ndiye Mulungu, palibe wina.


Pamenepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lake lonse, nadzaima pamaso pake, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu padziko lonse lapansi, koma kwa Israele ndiko; ndipo tsopano, mulandire chakukuyamikani nacho kwa mnyamata wanu.


Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu.


Ndi m'maiko monse, ndi m'mizinda yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lake, Ayuda anali nako kukondwera ndi chimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m'dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.


Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova, ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu.


Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.


Apitetu ngati madzi oyenda; popiringidza mivi yake ikhale yodukaduka.


Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.


Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira; kuda mtima kwagwira anthu okhala mu Filistiya.


Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa; agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu; okhala mu Kanani onse asungunuka mtima.


Chifukwa chake manja onse adzafooka, ndi mitima yonse ya anthu idzasungunuka;


Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.


Ndalozetsa nsonga ya lupanga kuzipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kuchuluke; ha! Analituula linyezimire, analisongoza liphe.


Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.


Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo aakulu ndi aatali akuposa ife; mizinda ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.


Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakuchita mantha ndi wofumuka mtima? Amuke nabwerere kunyumba kwake, ingasungunuke mitima ya abale ake monga mtima wake.


Potero dziwani lero lino nimukumbukire m'mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m'thambo la kumwamba ndi padziko lapansi; palibe wina.


Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.


Ndipo anati kwa Yoswa, Zoonadi, Yehova wapereka dziko lonse m'manja mwathu; ndiponso nzika zonse zasungunuka pamaso pathu.


Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele.


Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapirikitsa kuyambira pachipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.


Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi.


nanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife kunkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi kumkwiyo wa Mwanawankhosa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa