Yoswa 2:10 - Buku Lopatulika10 Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a mu Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka mu Ejipito; ndi chija munachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordani, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m'Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka m'Ejipito; ndi chija munachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordani, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Inde, tamva m'mene Chauta adaphwetsera Nyanja Yofiira inu mukufika, m'mene munkatuluka ku Ejipito. Tamvanso m'mene mudakanthira mafumu aŵiri a Aamori, Sihoni ndi Ogi, kuvuma kwa Yordani kuja. Mudakantha ndi magulu ao ankhondo omwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Ife tinamva mmene Yehova anawumitsira madzi a Nyanja Yofiira inu mukufika pamene munatuluka mʼdziko la Igupto. Tamvanso zimene munachita kwa Sihoni ndi Ogi, mafumu awiri a Aamori amene ali kummawa kwa Yorodani. Inu munawawononga kotheratu. Onani mutuwo |