Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 19:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo maere achiwiri anamtulukira Simeoni, fuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi cholowa chao chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo maere achiwiri anamtulukira Simeoni, fuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi cholowa chao chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mabanja a Simeoni adalandiranso gawo lao, Yoswa atachita maere kachiŵiri. Dziko lake linali m'kati mwenimweni mwa dziko la mabanja a Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Maere achiwiri anagwera mabanja a fuko la Simeoni. Dziko lawo linali mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 19:1
10 Mawu Ofanana  

ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;


Ndipo anakhala ku Beereseba, ndi Molada, ndi Hazara-Suwala,


Ndi kumalire a Benjamini, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Simeoni, gawo limodzi.


Ndipo mizinda ya ku malekezero a fuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwera ndiwo, Kabizeeli ndi Edere, ndi Yaguru;


ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.


Ndipo anali nacho cholowa chao Beereseba, kapena Sheba, ndi Molada;


M'gawo la ana a Yuda muli cholowa cha ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawachulukira; chifukwa chake ana a Simeoni anali nacho cholowa pakati pa cholowa chao.


Mwa fuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko Levi zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa