Yoswa 18:9 - Buku Lopatulika9 Namuka amunawo, napitapita pakati padziko, nalilemba m'buku, nayesa midzi yake, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku chigono ku Silo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Namuka amunawo, napitapita pakati pa dziko, nalilemba m'buku, nayesa midzi yake, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku chigono ku Silo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Pamenepo anthuwo adakaliyendera dziko lonselo, nalemba bwino m'buku za dzikolo. Adagaŵa dzikolo magawo asanu ndi aŵiri, ndipo adalembanso mndandanda wa midzi yonse. Atatero adabwerera kwa Yoswa ku zithando ku Silo kuja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Ndipo anthu anachoka ndi kukayendera dziko lonse. Iwo analemba bwinobwino mʼbuku za dzikolo, mzinda ndi mzinda. Analigawa magawo asanu ndi awiri, ndipo anabwerera kwa Yoswa ku misasa ya ku Silo. Onani mutuwo |