Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 17:6 - Buku Lopatulika

6 popeza ana aakazi a Manase adalandira cholowa pakati pa ana ake aamuna; ndi dziko la Giliyadi linakhala la ana a Manase otsala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 popeza ana akazi a Manase adalandira cholowa pakati pa ana ake amuna; ndi dziko la Giliyadi linakhala la ana a Manase otsala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 popeza kuti ana aakazi a Manase ndi ana ake aamuna, onsewo adalandira magawo ao. Dziko la Giliyadi lidapatsidwa kwa otsala mwa zidzukulu za Manase.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 chifukwa ana aakazi a fuko la Manase analandira cholowa chawo pakati pa ana aamuna. Dziko la Giliyadi linali dziko la zidzukulu zonse za Manase.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 17:6
7 Mawu Ofanana  

Ndi m'malire a Nafutali, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Manase, limodzi.


Mose anaperekanso cholowa kwa hafu la fuko la Manase, ndicho cha hafu la fuko la Manase monga mwa mabanja ao.


Ndipo malire ao anayambira ku Mahanaimu, Basani lonse, ufumu wonse wa Ogi mfumu ya ku Basani, ndi mizinda yonse ya Yairi, yokhala mu Basani, mizinda makumi asanu ndi limodzi;


ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi mu Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.


Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Giliyadi ndi Basani lokhala tsidya lija la Yordani:


Ndipo malire a Manase anayambira ku Asere, kunka ku Mikametati, wokhala chakuno cha Sekemu; namuka malire ku dzanja lamanja kwa nzika za Enitapuwa.


Ndipo gawo limodzi la fuko la Manase, Mose anawapatsa cholowa mu Basani; koma gawo lina Yoswa anawaninkha cholowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordani kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa