Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 17:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Giliyadi ndi Basani lokhala tsidya lija la Yordani:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Giliyadi ndi Basani lokhala tsidya lija la Yordani:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Choncho kuwonjeza pa maiko a Giliyadi ndi Basani a kuvuma kwa Yordani, a fuko la Manase adalandiranso magawo khumi,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Choncho kuwonjezera pa mayiko a Giliyadi ndi Basani kummawa kwa Yorodani, anthu a fuko la Manase analandiranso magawo khumi

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 17:5
9 Mawu Ofanana  

Ndi m'malire a Nafutali, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Manase, limodzi.


ndi Giliyadi, ndi malire a Agesuri, ndi Amaakati, ndi phiri lonse la Heremoni, ndi Basani lonse mpaka ku Saleka;


Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?


Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse cholowa pakati pa abale athu; chifukwa chake anawapatsa monga mwa lamulo la Yehova, cholowa pakati pa abale a atate wao.


popeza ana aakazi a Manase adalandira cholowa pakati pa ana ake aamuna; ndi dziko la Giliyadi linakhala la ana a Manase otsala.


Ndipo gawo limodzi la fuko la Manase, Mose anawapatsa cholowa mu Basani; koma gawo lina Yoswa anawaninkha cholowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordani kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa