Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 17:3 - Buku Lopatulika

3 Koma Zelofehadi, mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana aamuna koma ana aakazi ndiwo; ndipo maina a ana ake aakazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma Zelofehadi, mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana amuna koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana ake akazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Panali Zelofehadi mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase. Zelofehadiyo analibe mwana wamwamuna ndi mmodzi yemwe, koma aakazi okhaokha. Maina a ana aakaziwo ndi aŵa: Mahala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Panali Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri mwana wa Manase. Iyeyu analibe ana aamuna koma aakazi okhaokha ndipo mayina awo ndi awa: Mahila, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 17:3
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.


Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana aamuna, koma ana aakazi ndiwo; ndipo maina a ana aakazi a Zelofehadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.


Pamenepo anayandikiza ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake aakazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.


Ndipo maere anagwera ana ena otsala a Manase monga mwa mabanja ao; ana a Abiyezere ndi ana a Heleki, ndi ana a Asiriele, ndi ana a Sekemu ndi ana a Hefere, ndi ana a Semida; awa ndi ana aamuna a Manase mwana wa Yosefe, monga mwa mabanja ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa