Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 17:12 - Buku Lopatulika

12 Koma ana a Manase sanathe kuingitsa a m'mizinda aja, popeza Akanani anafuna kukhala m'dziko lija.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma ana a Manase sanathe kuingitsa a m'midzi aja, popeza Akanani anafuna kukhala m'dziko lija.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Komabe anthu a fuko la Manase sadathe kuŵapirikitsa Akanani okhala m'mizinda imeneyo. Motero Akananiwo adangokhalabe komweko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Komabe anthu a fuko la Manase sanathe kuwapirikitsa anthu okhala mʼmizinda imeneyi. Choncho Akanaani anakhalabe mʼmizindayi.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 17:12
7 Mawu Ofanana  

ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a Israele sanakhoze kuononga konse, Solomoni anawasenzetsa msonkho wa ntchito kufikira lero.


Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.


Ndipo sanaingitse Akanani akukhala mu Gezere; koma Akanani anakhala pakati pa Efuremu, kufikira lero lino, nawaumiriza kugwira ntchito yathangata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa