Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 14:2 - Buku Lopatulika

2 Cholowa chao chinachitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mafuko asanu ndi anai ndi fuko la hafu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Kulandira kwao kunachitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mafuko asanu ndi anai ndi fuko logawika pakati.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Potsata zimene Mulungu adalamula Mose, dziko lonse lidagaŵidwa mwamaere kwa mafuko asanu ndi anai ndi theka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Madera anagawidwa mwa maere kwa mafuko asanu ndi anayi ndi theka, monga momwe Yehova analamulira kudzera mwa Mose.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 14:2
14 Mawu Ofanana  

Maere aponyedwa pamfunga; koma ndiye Yehova alongosola zonse.


Maere aletsa makangano, nulekanitsa amphamvu.


Ndipo pogawa dziko likhale cholowa chao, mupereke chopereka kwa Yehova, ndicho gawo lopatulika la dziko; m'litali mwake likhale la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m'malire ake onse pozungulira pake.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu.


Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;


Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale cholowa chanu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni.


Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:


Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.


Ndipo tsopano uwagawire mafuko asanu ndi anai, ndi hafu la fuko la Manase, dziko ili likhale cholowa chao.


Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao.


Ndipo muzilemba dziko likhale magawo asanu ndi awiri, ndi kubwera nao kuno kwa ine malembo ake; ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa