Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 13:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo tsopano uwagawire mafuko asanu ndi anai, ndi hafu la fuko la Manase, dziko ili likhale cholowa chao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo tsopano uwagawire mafuko asanu ndi anai, ndi fuko la Manase logawika pakati, dziko ili likhale cholowa chao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono ugaŵe maiko ameneŵa pakati pa mafuko asanu ndi anai ndi theka lina lija la fuko la Manase, kuti akhale choloŵa chao.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Tsopano ugawire dziko limeneli mafuko asanu ndi anayi ndiponso theka la fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 13:7
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anawapatsa maiko a amitundu; iwo ndipo analanda zipatso za ntchito ya anthu:


Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao.


Ndipo pogawa dziko likhale cholowa chao, mupereke chopereka kwa Yehova, ndicho gawo lopatulika la dziko; m'litali mwake likhale la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m'malire ake onse pozungulira pake.


Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu.


Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;


nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira.


Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;


Cholowa chao chinachitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mafuko asanu ndi anai ndi fuko la hafu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa