Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 13:2 - Buku Lopatulika

2 Dziko lotsala ndilo: malire onse a Afilisti, ndi Agesuri onse,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Dziko lotsala ndilo: malire onse a Afilisti, ndi Agesuri onse,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Maiko amene atsalako ndi aŵa: dziko lonse la Afilisti, ndi dziko lonse la Gesuri,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Madera amene atsala ndi awa: chigawo chonse cha Afilisti ndi Agesuri

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 13:2
15 Mawu Ofanana  

ndi Patirusimu, ndi Kasiluhimu, m'menemo ndipo anatuluka Afilisti, ndi Kafitori.


Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isaki ananka kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari.


Pakuti mnyamata wanu ndinawinda pakukhala ine ku Gesuri mu Aramu, ndi kuti, Yehova akadzandibwezeranso ndithu ku Yerusalemu, ine ndidzatumikira Yehova.


wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri;


Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Filistiya? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu.


Tsoka, okhala m'dziko la kunyanja, mtundu wa Akereti! Mau a Yehova atsutsana nawe, Kanani, dziko la Afilisti; ndidzakuononga, kuti pasakhale wokhala m'dziko.


Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino).


nachita ufumu m'phiri la Heremoni, ndi mu Saleka, ndi mu Basani lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Giliyadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni.


ndi Giliyadi, ndi malire a Agesuri, ndi Amaakati, ndi phiri lonse la Heremoni, ndi Basani lonse mpaka ku Saleka;


Koma ana a Israele sanainge Agesuri kapena Amaakati; koma Gesuri, ndi Maakati amakhala pakati pa Israele, mpaka lero lino.


Ndipo iyo ndiyo mitundu ya anthu anaisiyapo Yehova kuyesa nayo Israele, ndiwo onse amene sanadziwe nkhondo zonse za Kanani;


Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa