Yoswa 13:12 - Buku Lopatulika12 ufumu wonse wa Ogi mu Basani, wa kuchita ufumu mu Asitaroti, ndi mu Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 ufumu wonse wa Ogi m'Basani, wa kuchita ufumu m'Asitaroti, ndi m'Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Ndipo ku Basani lidaphatikizapo dziko la Ogi amene ankalamula ku Asitaroti ndi ku Ederei. (Ogi anali yekhayo mfumu ya Arefaimu amene adatsalako). Mose anali atagonjetseratu anthu ameneŵa ndi kuŵapirikitsira kutali. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Linaphatikizanso dziko la mfumu Ogi ya ku Basani imene imalamulira kuchokera ku Asiteroti ndi Ederi. Iye yekha ndiye anali mfumu ya Arefaimu amene anapulumuka. Mose anali atawagonjetsa anthu amenewa ndi kuwathamangitsira kutali. Onani mutuwo |