Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 12:8 - Buku Lopatulika

8 kumapiri ndi kuchigwa, ndi kuchidikha, ndi kumatsikiro, ndi kuchipululu, ndi kumwera: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 kumapiri ndi kuchigwa, ndi kuchidikha, ndi kumatsikiro, ndi kuchipululu, ndi kumwera: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Dziko limenelo lidaali lamapiri, lachipululu, ndiponso dziko louma lakumwera. M'dziko limeneli ndimo m'mene munkakhala Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 12:8
14 Mawu Ofanana  

ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini;


Ndipo Abramu anayenda ulendo wake, nayendayenda kunka kumwera.


Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti. Akanani ndi Aperizi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo.


Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawaononga.


ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.


Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;


Imvani Israele; mulikuoloka Yordani lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akulu ndi amphamvu akuposa inu, mizinda yaikulu ndi ya malinga ofikira kuthambo,


Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwera, la kuchidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyepo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israele adalamulira.


Motero Yoswa analanda dziko lonselo, la kumapiri, ndi la kumwera, ndi dziko lonse la Goseni, ndi dziko la kuchidikha, ndi la kuchigwa; ndi la kumapiri la Israele, ndi la ku chidikha chake;


Nati Yoswa, Ndi ichi mudzadziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati pa inu, ndi kuti adzapirikitsa ndithu pamaso panu Akanani, ndi Ahiti, ndi Ahivi, ndi Aperizi, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Ayebusi.


Ndipo kunali, pakumva ichi mafumu onse a tsidya ilo la Yordani, kumapiri ndi kuchidikha, ndi ku madooko onse a Nyanja Yaikulu, pandunji pa Lebanoni: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;


Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwera ndi kuchidikha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa