Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 12:2 - Buku Lopatulika

2 Sihoni mfumu ya Aamori wokhala mu Hesiboni, wochita ufumu kuyambira ku Aroere ndiwo m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi pakati pa chigwa ndi pa Giliyadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Sihoni mfumu ya Aamori wokhala m'Hesiboni, wochita ufumu kuyambira ku Aroere ndiwo m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi pakati pa chigwa ndi pa Giliyadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Sihoni mfumu ya Aamori amene ankakhala ku Hesiboni. Iyeyu ankalamulira kuyambira ku Aroere, mzinda umene uli pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki ku malire a dziko la Aamoni, ndiponso kuphatikizapo theka la dera la Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 12:2
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ake awiri, ndi adzakazi ake awiri, ndi ana ake aamuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa dooko la Yaboki.


ndi Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yowele, wokhala ku Aroere, ndi kufikira ku Nebo ndi Baala-Meoni;


Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale laolao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.


Sihoni mfumu ya Aamori, ndi Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a Kanani:


Iwe wokhala mu Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani?


atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, wakukhala mu Asitaroti, ku Ederei.


Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Chifukwa Israele analanda dziko langa pakukwera iye kuchokera ku Ejipito, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordani; ndipo tsopano undibwezere maikowa mwamtendere.


Ndipo analandira akhale cholowa chao, malire onse a Aamori, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi kuyambira chipululu mpaka Yordani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa