Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 11:6 - Buku Lopatulika

6 Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; udzawadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; uziwadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Chauta adauza Yoswa kuti, “Usaŵaope amenewo. Maŵa pa nthaŵi yonga yomwe ino, adzaphedwa onsewo. Akavalo ao muŵalumaze, ndipo mutenthe magaleta ao.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope chifukwa mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzawapereka kuti muwaphe. Akavalo awo muwadule matsinde ndipo magaleta awo muwatenthe ndi moto.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 11:6
24 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anatenga apakavalo ake chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magaleta, koma anasunga a iwo akufikira magaleta zana limodzi.


Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.


Mawa muwatsikire; taonani, akwera pokwerera pa Zizi, mudzakomana nao polekezera chigwa chakuno cha chipululu cha Yeruwele.


Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.


Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.


Wolungama woyenda mwangwiro, anake adala pambuyo pake.


Koma munati, Iai, pakuti tidzathawa pa akavalo; chifukwa chake inu mudzathawadi; ndipo ife tidzakwera pa akavalo aliwiro; chifukwa chake iwo amene akuthamangitsani, adzakhala aliwiro.


Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!


Ndipo iwo okhala m'mizinda ya Israele adzatuluka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zotchinjiriza, mauta, ndi mivi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;


Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo.


Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magaleta ake mu utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzachotsa zofunkha zako padziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso.


Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha.


Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako.


Ndipo mafumu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israele nkhondo.


Ndipo Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo naye, anawadzera modzidzimutsa ku madzi a Meromu, nawagwera.


Ndipo Yoswa anawachitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magaleta ao ndi moto.


Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati pa inu.


namaima ku likasalo Finehasi mwana wa Eleazara mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditulukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke? Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako.


Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako.


Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona chipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabesi; nakondwera iwowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa