Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 11:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anatuluka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kuchuluka kwao ngati mchenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magaleta ambirimbiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anatuluka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kuchuluka kwao ngati mchenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magaleta ambirimbiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mafumuwo adabwera ndi ankhondo ao onse, ndipo kuchuluka kwao kwa ankhondowo kunali ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Anali ndi akavalo ambiri, pamodzi ndi magaleta omwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mafumuwo anabwera pamodzi ndi ankhondo awo onse. Gulu la ankhondo linali lalikulu ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Analinso ndi akavalo ndi magaleta ambiri.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 11:4
8 Mawu Ofanana  

kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;


Ndipo Inu munati, Ndidzakuchitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbeu yako monga mchenga wa pa nyanja, umene sungathe kuwerengeka chifukwa cha unyinji wake.


Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake.


Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.


Iwowa anagonjeka, nagwa; koma ife tauka, ndipo takhala chilili.


Ndipo mafumu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israele nkhondo.


Ndipo Amidiyani ndi Aamaleke ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'chigwa, kuchuluka kwao ngati dzombe; ndi ngamira zao zosawerengeka, kuchuluka kwao ngati mchenga wa m'mphepete mwa nyanja.


Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa