Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 10:2 - Buku Lopatulika

2 anaopa kwambiri, popeza Gibiyoni ndi mzinda waukulu, monga wina wa mizinda yachifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwake, ndi amuna ake onse ndiwo amphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 anaopa kwambiri, popeza Gibiyoni ndi mudzi waukulu, monga wina wa midzi yachifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwake, ndi amuna ake onse ndiwo amphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Motero anthu a ku Yerusalemu adachita mantha kwambiri, pakuti Gibiyoni unali mzinda waukulu, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu kupambana Ai, ndipo ankhondo ake anali olimba mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Choncho iye ndi anthu ake anachita mantha aakulu, chifukwa Gibiyoni unali mzinda waukulu kwambiri, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu ndipo ankhondo ake anali olimba mtima.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 10:2
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mzinda wachifumu.


Chomwe woipa achiopa chidzamfikira; koma chomwe olungama achifuna chidzapatsidwa.


Palibe munthu adzaima pamaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, chifukwa cha inu, monga anenana ndi inu.


Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.


Ndipo anthu onse a padziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.


koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.


Kugwa m'manja a Mulungu wamoyo nkoopsa.


Ndipo anati kwa Yoswa, Zoonadi, Yehova wapereka dziko lonse m'manja mwathu; ndiponso nzika zonse zasungunuka pamaso pathu.


Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi.


Koma pamene nzika za Gibiyoni zinamva zimene Yoswa adachitira Yeriko ndi Ai,


Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kuminda, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji mu mzinda wachifumu pamodzi ndi inu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa