Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 10:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m'phanga la ku Makeda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m'phanga la ku Makeda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Mafumu asanu onse aja adathaŵa nakabisala ku phanga ku Makeda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mafumu asanu aja anathawa ndi kukabisala ku phanga la Makeda.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 10:16
17 Mawu Ofanana  

Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa, ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.


Pogona inu m'makola a zoweta, mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.


Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko.


Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe.


Pamenepo Yoswa anabwezera, ndi Aisraele onse pamodzi naye, ku chigono cha ku Giligala.


Ndipo anauza Yoswa ndi kuti, Mafumu asanuwa apezeka obisala m'phanga la ku Makeda.


Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo.


Ndipo mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;


Pamene dzanja la Midiyani linagonjetsa Israele, ana a Israele anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga chifukwa cha Midiyani.


Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.


Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Saulo analowa kuti akadzithandize. Ndipo Davide ndi anyamata ake analikukhala m'kati mwa phangamo.


Bwino lake Davide yemwe ananyamuka, natuluka m'phangamo, nafuulira Saulo, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakucheuka Saulo, Davide anaweramira nkhope yake pansi, namgwadira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa