Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 10:12 - Buku Lopatulika

12 Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele; ndipo anati pamaso pa Israele, Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni, ndi Mwezi iwe, m'chigwa cha Ayaloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele; ndipo anati pamaso pa Israele, Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni, ndi Mwezi iwe, m'chigwa cha Ayaloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pa tsiku limene Chauta adapatsa Aisraele mphamvu kuti agonjetse Aamori, Yoswa adalankhula naye. Tsono pamaso pa Aisraele onse adati, “Iwe dzuŵa, ima pamwamba pa Gibiyoni, iwe mwezi, ima pamwamba pa chigwa cha Ayaloni.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori mʼmanja mwa Israeli, Yoswa ananena kwa Yehova pamaso pa Israeli kuti, “Iwe dzuwa, ima pamwamba pa Gibiyoni, mwezi ima pamwamba pa chigwa cha Ayaloni.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 10:12
29 Mawu Ofanana  

Ndipo Abinere mwana wa Nere ndi anyamata a Isiboseti mwana wa Saulo anatuluka ku Mahanaimu kunka ku Gibiyoni.


Nati Hezekiya, Kutsikira mthunzi makwerero khumi nkopepuka, kutero ai; koma mthunzi ubwerere makwerero khumi.


Nafuulira kwa Yehova Yesaya mneneriyo, nabweza Iye mthunzi m'mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi.


Nati Yesaya, Chizindikiro ndichi akupatsa Yehova, kuti Yehova adzachichita chonena Iye; kodi mthunzi umuke m'tsogolo makwerero khumi, kapena ubwerere m'mbuyo makwerero khumi?


ndi Beriya, ndi Sema; ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo okhala mu Ayaloni, amene anathawitsa okhala mu Gati;


ndi Zora, ndi Ayaloni, ndi Hebroni; ndiyo mizinda yamalinga ya mu Yuda ndi Benjamini.


Amene alamulira dzuwa ndipo silituluka, nakomera nyenyezi chizindikiro chakuzitsekera.


Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira.


Muyeso wao wapitirira padziko lonse lapansi, ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu. Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,


Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu, munakonza kuunika ndi dzuwa.


Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'chigwa cha Gibiyoni; kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo, ndi kuti achite chochita chake, chochita chake chachilendo.


taona, ndidzabweza mthunzi wa pamakwerero, umene watsika pa makwerero a Ahazi ndi dzuwa, ubwerere makwerero khumi. Ndipo dzuwa linabwerera makwerero khumi pamakwerero, pamene udatsika mthunziwo.


Dzuwa lako silidzalowanso, mwezi wako sudzanka kumidima; pakuti Yehova adzakhala kuunika kwako kosatha, ndi masiku a kulira maliro ako adzatha.


Ndipo panali chaka chomwecho, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, chaka chachinai, mwezi wachisanu, kuti Hananiya mwana wa Azuri mneneri, amene anali wa ku Gibiyoni, ananena ndi ine m'nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti,


Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m'mwamba, ndi mizu yao pansi.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Ambuye Yehova, ndidzalowetsa dzuwa usana, ndi kudetsa dziko pausana poyera.


Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.


Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao; pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo. Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.


Khalani chete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwake mopatulika.


nakatumikira milungu ina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine;


ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.


Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima mpaka anthu adabwezera chilango adani ao. Kodi ichi sichilembedwa m'buku la Yasara? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.


Saalabini, ndi Ayaloni ndi Itila;


Ayaloni ndi mabusa ake, Gatirimoni ndi mabusa ake; mizinda inai.


Nafa Eloni Mzebuloni naikidwa mu Ayaloni m'dziko la Zebuloni.


Nyenyezi zinathira nkhondo yochokera kumwamba, m'mipita mwao zinathirana ndi Sisera.


Momwemo Samuele anaitana kwa Yehova; ndipo Yehova anatumiza bingu ndi mvula tsiku lomwelo; ndipo anthu onse anaopa kwambiri Yehova ndi Samuele.


Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ayaloni, ndipo anthu anafooka kwambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa