Yoswa 10:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nachitira Ai ndi mfumu yake monga adachitira Yeriko ndi mfumu yake; ndi kuti nzika za Gibiyoni zinachitirana mtendere ndi Israele, n'kukhala pakati pao; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nachitira Ai ndi mfumu yake monga adachitira Yeriko ndi mfumu yake; ndi kuti nzika za Gibiyoni zinachitirana mtendere ndi Israele, nizikhala pakati pao; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Adonizedeki mfumu ya ku Yerusalemu adamva kuti Yoswa wagonjetsa kotheratu mzinda wa Ai, ndipo waononga mzindawo pamodzi ndi mfumu yake, monga momwe adachitira Yeriko pamodzi ndi mfumu yake yomwe. Adamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni adapangana za mtendere ndi Aisraele, ndipo kuti anali kukhala pakati pao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Adoni-Zedeki mfumu ya ku Yerusalemu inamva kuti Yoswa wagonjetsa ndi kuwononga kotheratu mzinda wa Ai pamodzi ndi mfumu yake, monga anachitira ndi Yeriko ndi mfumu yake. Inamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni anachita pangano la mtendere ndi Israeli ndipo amakhala pakati pawo. Onani mutuwo |