Yoswa 1:6 - Buku Lopatulika6 Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale cholowa chao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale cholowa chao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima, chifukwa udzatsogolera anthu ameneŵa pokalandira dziko limene ndidalonjeza kwa makolo ao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 “Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima, chifukwa iwe udzatsogolera anthu awa kukalandira dziko limene Ine ndinalonjeza makolo awo kuti ndidzawapatsa. Onani mutuwo |
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.