Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 4:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kumlanditsa m'nsautso yake. Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kumlanditsa m'nsautso yake. Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono Chauta Mulungu adameretsa msatsi kuti uchitire Yona mthunzi ndi kumchotsa mavuto ake. Yona adakondwa kwambiri chifukwa cha msatsiwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Tsono Yehova Mulungu anameretsa msatsi ndi kuyikulitsa kuti ipereke mthunzi kwa Yona kuchotsa mavuto ake; ndipo Yona anasangalala kwambiri chifukwa cha msatsiyo.

Onani mutuwo Koperani




Yona 4:6
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Hamani anatuluka tsiku lomwelo wosekerera ndi wokondwera mtima; koma pamene Hamani anapenya Mordekai kuchipata cha mfumu, osamnyamukira kapena kumfumukira, Hamani anadzazidwa ndi mkwiyo pa Mordekai.


Monga kapolo woliralira mthunzi, monga wolembedwa ntchito ayembekezera mphotho yake,


Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.


Ndipo Hezekiya anakondwera nao, nawaonetsa nyumba yake ya chuma, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsera, ndi nyumba yonse ya zida zake, ndi zonse zopezedwa m'zosungira zake; munalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena m'dziko lake lonse, kamene Hezekiya sanawaonetse.


inu okondwera nacho chopanda pake, ndi kuti, Kodi sitinadzilimbitse tokha ndi kulanda Karinaimu mwa mphamvu yathuyathu?


Koma Yehova anaikiratu chinsomba chachikulu chimeze Yona; ndipo Yona anali m'mimba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku.


Pamenepo Yona anatuluka m'mzinda, nakhala pansi kum'mawa kwa mzinda, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pake mumthunzi mpaka adzaona chochitikira mzinda.


Koma Mulungu anauikira mphanzi pakucha m'mawa mwake, ndiyo inadya msatsi, nufota.


Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa mu Mwamba.


ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa