Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 4:5 - Buku Lopatulika

5 Pamenepo Yona anatuluka m'mzinda, nakhala pansi kum'mawa kwa mzinda, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pake mumthunzi mpaka adzaona chochitikira mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pamenepo Yona anatuluka m'mudzi, nakhala pansi kum'mawa kwa mudzi, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pake mumthunzi mpaka adzaona chochitikira mudzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Yona adatuluka mumzindamo nakakhala pansi chakuvuma kwake. Kumeneko adadzimangira chithando nakhala m'menemo mu mthunzi, kudikira kuti aone zimene zichitike mumzindamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yona anatuluka mu mzindamo nakakhala pansi cha kummawa kwa mzindawo. Kumeneko anadzimangira chithando nakhala mʼmenemo mu mthunzi, kudikira kuti aone zimene zichitikire mzindawo.

Onani mutuwo Koperani




Yona 4:5
10 Mawu Ofanana  

Ndipo atamva Eliya, anafunda nkhope yake ndi chofunda chake, natuluka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Uchitanji kuno, Eliya?


Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Uchitanji pano, Eliya?


Chifukwa cha kuipa kwa kusirira kwake ndinakwiya ndi kummenya iye; ndinabisa nkhope yanga, ndipo ndinakwiya; ndipo iye anankabe mokhota m'njira ya mtima wake.


Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.


Pamenepo amalinyero anachita mantha, nafuulira yense kwa mulungu wake, naponya m'nyanja akatundu anali m'chombo kuchipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa chombo, nagona tulo tofa nato.


Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi?


Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kumlanditsa m'nsautso yake. Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa