Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 4:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirepo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirapo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Chauta adati, “Iwe ukumvera chisoni msatsi umene sudaugwirire ntchito, sindiwe udaubzala ndi kuukuza. Udamera pa usiku umodzi, nufanso pa usiku umodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma Yehova anati, “Iwe ukumvera chisoni msatsiwo, ngakhale kuti sunawugwirire ntchito kapena kuwukulitsa. Inamera pa usiku umodzi ndipo inafanso pa usiku umodzi.

Onani mutuwo Koperani




Yona 4:10
4 Mawu Ofanana  

A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana aamuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.


ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?


Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.


Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa