Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 3:8 - Buku Lopatulika

8 koma zifundidwe ndi chiguduli munthu ndi nyama, ndipo zifuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yake yoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 koma zifundidwe ndi chiguduli munthu ndi nyama, nizifuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yake yoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Anthu avale ziguduli, nyamanso aziveke ziguduli. Anthuwo azifuula kwa Mulungu ndi mphamvu zao zonse. Ndithu aliyense asiye makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zankhanza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma anthu avale ziguduli, ndipo nyamanso aziveke ziguduli. Munthu aliyense azifuwula kwa Mulungu ndi mphamvu zake zonse. Anthuwo asiye makhalidwe awo oyipa ndi machitidwe achiwawa.

Onani mutuwo Koperani




Yona 3:8
23 Mawu Ofanana  

pangakhale palibe chiwawa m'manja mwanga, ndi pemphero langa ndi loyera.


Awatseguliranso m'khutu mwao kuti awalangize, nawauza abwerere kuleka mphulupulu.


Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse?


Maukonde ao sadzakhala zovala, sadzafunda ntchito zao; ntchito zao zili ntchito zoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwao.


Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu choipa, ndilingalira inu kanthu kakuchitira inu choipa; mubwerere tsono inu nonse, yense kunjira yake yoipa, nimukonze njira zanu ndi machitidwe anu.


ndi kuti, Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yake yoipa, ndi zoipa za ntchito zanu, ndi kukhala m'dziko limene Yehova anapatsa inu ndi makolo anu, kuyambira kale kufikira muyaya;


Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yake yoipa; kuti ndileke choipa, chimene ndinati ndiwachitire chifukwa cha kuipa kwa ntchito zao.


Kapena nyumba ya Yuda idzamva choipa chonse chimene nditi ndidzawachitire; kuti abwerere yense kuleka njira yake yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi tchimo lao.


Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?


Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphawi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.


Patulani tsiku losala, lalikirani misonkhano yoletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m'dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.


Pamenepo anafuulira kwa Yehova, nati, Tikupemphanitu, Yehova, tisatayike chifukwa cha moyo wa munthu uyu, musatisenzetse mwazi wosachimwa; pakuti, Inu Yehova, mwachita monga mudakomera Inu.


Ndipo mwini chombo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? Uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukira tingatayike.


Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima:


komatu kuyambira kwa iwo a mu Damasiko, ndi a mu Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.


Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;


Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa