Yona 3:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo analalikira, nanena mu Ninive mwa lamulo la mfumu ndi nduna zake, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo analalikira, nanena m'Ninive mwa lamulo la mfumu ndi nduna zake, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Tsono mfumuyo idalengeza ku Ninive, kuti, “Nali lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: ‘Munthu aliyense asadye kanthu, ndiponso ziŵeto zonse zikuluzikulu ndi zing'onozing'ono zomwe zisadye kanthu. Zisadyetu kanthu, nkumwa madzi komwe zisamwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Tsono mfumuyo inalengeza mu Ninive kuti, “Mwa lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: “Munthu aliyense kapenanso nyama, ngʼombe kapena nkhosa, zisadye kanthu kalikonse; musazilole kuti zidye kapena kumwa. Onani mutuwo |