Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 3:6 - Buku Lopatulika

6 Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Ninive, ndipo inanyamuka kumpando wake wachifumu, nivula chofunda chake, nifunda chiguduli, nikhala m'maphulusa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Ninive, ndipo inanyamuka kumpando wake wachifumu, nivula chofunda chake, nifunda chiguduli, nikhala m'maphulusa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Mfumu ya ku Ninive itamva zimenezo, idatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake. Idavala chiguduli, nikakhala nao pa dzala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mfumu ya ku Ninive itamva nkhaniyi, inatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake waufumu ndipo inavala chiguduli ndi kukhala pansi pa fumbi.

Onani mutuwo Koperani




Yona 3:6
20 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zovala zake, navala chiguduli pathupi pake, nasala kudya, nagona pachiguduli, nayenda nyang'anyang'a.


Ndipo anadzitengera phale, kudzikanda nalo; nakhala pansi m'maphulusa.


chifukwa chake ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m'fumbi ndi mapulusa.


M'makwalala mwao adzimangira chiguduli m'chuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m'malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri.


Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.


Ndipo Mikaya anafotokozera iwo mau onse amene anamva, pamene Baruki anawerenga buku m'makutu a anthu.


Ndipo sanaope, sanang'ambe nsalu zao, kapena mfumu, kapena atumiki ake aliyense amene anamva mau onsewa.


Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kumvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.


Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola; aponya fumbi pa mitu yao, anamangirira chiguduli m'chuuno mwao: Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.


Aike kamwa lake m'fumbi; kapena chilipo chiyembekezo.


Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yachifumu yao, nadzavula zovala zao zopikapika, nadzavala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kudabwa nawe.


Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.


Musachifotokoza mu Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'fumbi.


Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Tiro ndi mu Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.


Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika mu Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa