Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 1:5 - Buku Lopatulika

5 Pamenepo amalinyero anachita mantha, nafuulira yense kwa mulungu wake, naponya m'nyanja akatundu anali m'chombo kuchipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa chombo, nagona tulo tofa nato.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pamenepo amalinyero anachita mantha, nafuulira yense kwa mulungu wake, naponya m'nyanja akatundu anali m'chombo kuchipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa chombo, nagona tulo tofa nato.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Amalinyero adachita mantha, aliyense nkumalirira mulungu wake. Adayamba kuponya katundu m'nyanja kuti chombo chipepuke. M'menemo nkuti Yona atatsikira m'katikati mwa chombo, ali m'tulo tofa nato.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Onse oyendetsa sitimayo anachita mantha ndipo aliyense anayamba kupemphera kwa mulungu wake. Ndipo anaponya katundu mʼnyanja kuti sitimayo ipepuke. Koma Yona pa nthawiyi nʼkuti atatsikira mʼkatikati mwa sitimayo kumene anagona tulo tofa nato.

Onani mutuwo Koperani




Yona 1:5
22 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anatenga ng'ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m'mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wovomereza. Ndipo anavinavina kuguwa adalimanga.


Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.


Popeza anena, nautsa namondwe, amene autsa mafunde ake.


moto ndi matalala, chipale chofewa ndi nkhungu; mphepo ya namondwe, yakuchita mau ake;


mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika; mphindi yakusunga ndi mphindi yakutaya;


Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani chifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mulungu wosakhoza kupulumutsa.


Koma ili kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kuvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa mizinda yako, Yuda iwe.


Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.


Pamenepo anafuulira kwa Yehova, nati, Tikupemphanitu, Yehova, tisatayike chifukwa cha moyo wa munthu uyu, musatisenzetse mwazi wosachimwa; pakuti, Inu Yehova, mwachita monga mudakomera Inu.


Ndipo amunawo anaopa Yehova ndi mantha aakulu, namphera Yehova nsembe, nawinda.


Ndipo mwini chombo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? Uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukira tingatayike.


Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo.


Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m'tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo.


Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a ochimwa.


Ndipo m'mene anakhuta, anapepuza ngalawa, nataya tirigu m'nyanja.


Pamenepo anamgonetsa pa mabondo ake, naitana munthu, nameta njombi zake zisanu ndi ziwiri; nayamba kumzunza, nimchokera mphamvu yake.


Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Saulo analowa kuti akadzithandize. Ndipo Davide ndi anyamata ake analikukhala m'kati mwa phangamo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa