Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 1:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo anati nao, Mundinyamule ndi kundiponya m'nyanja, momwemo nyanja idzachitira inu bata; pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkulu amene wakugwerani chifukwa cha ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo anati nao, Mundinyamule ndi kundiponya m'nyanja, momwemo nyanja idzachitira inu bata; pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkulu amene wakugwerani chifukwa cha ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Yonayo adaŵauza kuti, “Chabwino, ingondiponyani m'nyanjamu, mukatero nyanjayi ikhala bata. Ndikudziŵa kuti wolakwa ndine, nkuwona namondweyu akukuvutani chotere.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Iye anayankha kuti, “Nyamuleni ndi kundiponya mʼnyanjamu ndipo nyanjayi ikhala bata. Ndikudziwa kuti wolakwa ndine nʼchifukwa chake chimphepo champhamvuchi chabwera pa inu.”

Onani mutuwo Koperani




Yona 1:12
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndachimwa ine, ndinachita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.


Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndachimwa ndi kuchita choipa ndithu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, linditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma lisatsutse anthu anu ndi kuwachitira mliri.


Choipa chanu chikhoza kuipira munthu wonga inu, ndi chilungamo chanu chikhoza kukomera wobadwa ndi munthu.


Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wochimwa mmodzi aononga zabwino zambiri.


Tsono anati kwa iye, Tichitenji nawe, kuti nyanja itichitire bata? Popeza namondwe anakulakulabe panyanja.


Koma amunawo anapalasa kubwerera kumtunda, koma sanathe; pakuti namondwe wa panyanja anakulakula mokomana nao.


kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usaonongeke.


nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.


Mwa ichi ana a Israele sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho, kuchichotsa pakati pa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa