Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 1:10 - Buku Lopatulika

10 Pamenepo amunawo anaopa kwambiri, nati kwa iye, Ichi nchiyani wachichita? Pakuti amunawo anadziwa kuti anathawa pamaso pa Yehova, popeza adawauza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pamenepo amunawo anaopa kwambiri, nati kwa iye, Ichi nchiyani wachichita? Pakuti amunawo anadziwa kuti anathawa pamaso pa Yehova, popeza adawauza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pamenepo amalinyero aja adachita mantha kwambiri, namufunsa kuti, “Kodi wachita chiyani?” Kudziŵa adaadziŵa kuti Yona ankathaŵa Chauta, poti anali ataŵauza kale.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Izi zinawachititsa mantha kwambiri ndipo anafunsa kuti, “Kodi wachita chiyani?” (Iwo ankadziwa kuti iyeyo amathawa Yehova, chifukwa nʼkuti atawawuza kale).

Onani mutuwo Koperani




Yona 1:10
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.


Ndipo Yowabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwachulukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu achione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi chinthu ichi?


Pakuti Mulungu adzamponyera zoopsa, osamleka; kuthawa akadathawa m'dzanja lake.


Tsono anati kwa iye, Tichitenji nawe, kuti nyanja itichitire bata? Popeza namondwe anakulakulabe panyanja.


Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova.


Ndipo pamene Pilato anamva mau awa, anaopa koposa.


Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa