Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 8:33 - Buku Lopatulika

33 Anamyankha iye, Tili mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhale akapolo a munthu nthawi iliyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa afulu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Anamyankha iye, Tili mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iliyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa afulu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Iwo adati, “Ife ndife ana a Abrahamu, ndipo chikhalire chathu sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Nanga bwanji ukuti, ‘Mudzasanduka aufulu?’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Iwo anamuyankha Iye kuti, “Ife ndife zidzukulu za Abrahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Kodi mukunena bwanji kuti, ‘Ife tidzamasulidwa?’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 8:33
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo zidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;


Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathu, natifikitsira chifundo pamaso pa mafumu a Persiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wake, ndi kutipatsa linga mu Yuda ndi mu Yerusalemu.


Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo.


ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.


Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.


Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala.


Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamu; koma mufuna kundipha Ine, chifukwa mau anga alibe malo mwa inu.


Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu.


Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa ninji? Chifukwa simungathe kumva mau anga.


kapena chifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isaki, mbeu yako idzaitanidwa.


Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele ndipo anawagulitsa m'dzanja la Kusani-Risataimu, mfumu ya Mesopotamiya; ndi ana a Israele anatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu.


Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa