Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 8:28 - Buku Lopatulika

28 Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Tsono Yesu adaŵauza kuti, “Mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Ndilipo. Mudzadziŵanso kuti sindichita kanthu pandekha, ndimalankhula zimene Atate adandiphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Choncho Yesu anati, “Inu mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziwa kuti Ine Ndine. Mudzadziwa kuti sindichita kalikonse pa Ine ndekha koma ndimayankhula zokhazo zimene Atate anandiphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 8:28
28 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.


Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.


Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasocheretsa ambiri.


Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.


Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.


Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene.


za chilungamo, chifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso;


kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene akuti adzafa nayo.


kumene anampachika Iye; ndipo pamodzi ndi Iye awiri ena, chakuno ndi chauko, koma Yesu pakati.


Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiona; ndipo umboni wathu simuulandira.


Ndipo monga Mose anakweza njoka m'chipululu, chotero Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa;


Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene.


Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu ndinena kwa inu, sangathe Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo.


Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.


Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.


Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.


Sanazindikira iwo kuti analikunena nao za Atate.


Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.


Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.


Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.


amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Khristu Ambuye wathu;


Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale ao, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mau anga m'kamwa mwake, ndipo adzanena nao zonse ndimuuzazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa