Yohane 7:35 - Buku Lopatulika35 Chifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzamuka kwa Agriki obalalikawo, ndi kuphunzitsa Agriki? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201435 Chifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzamuka kwa Agriki obalalikawo, ndi kuphunzitsa Agriki? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa35 Pamenepo akulu a Ayudawo adayamba kufunsana kuti, “Kodi iyeyu afuna kupita kuti kumene ife sitingakampeze? Kodi kapena akufuna kupita kwa anzathu amene adabalalikira kwa anthu a mitundu ina? Monga nkuti afuna kukaphunzitsa anthu akunja? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero35 Ayuda anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi munthu uyu akuganizira zoti apite kuti kumene ife sitingathe kumupeza Iye? Kodi Iye adzapita kumene anthu amakhala mobalalikana pakati pa Agriki, ndi kuphunzitsa Agriki? Onani mutuwo |