Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 6:64 - Buku Lopatulika

64 Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

64 Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

64 Koma pali ena mwa inu amene sakukhulupirira.” (Pakuti Yesu adaadziŵiratu mpachiyambi pomwe amene sadzakhulupirira, adaamudziŵiratunso amene analikudzampereka kwa adani ake.)

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

64 Komabe alipo ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Pakuti Yesu ankadziwa kuyambira pachiyambi ena mwa iwo amene samakhulupirira ndi amene adzamupereka Iye.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 6:64
20 Mawu Ofanana  

Simoni Mkanani, ndi Yudasi Iskariote amenenso anampereka Iye.


Koma inu simukhulupirira, chifukwa simuli a mwa nkhosa zanga.


Pamenepo Yesu, podziwa zonse zilinkudza pa Iye, anatuluka, nati kwa iwo, Mufuna yani?


Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu nokha.


Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira.


Pamenepo ambiri a ophunzira ake, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?


Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti ophunzira ake alikung'ung'udza chifukwa cha ichi, anati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho?


Pa ichi ambiri a ophunzira ake anabwerera m'mbuyo, ndipo sanayendeyendenso ndi Iye.


Ndipo ananena nao, Inu ndinu ochokera pansi; Ine ndine wochokera Kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindili Ine wa dziko lino lapansi.


ndipo inu simunamdziwe Iye; koma Ine ndimdziwa Iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa Iye, ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu; koma ndimdziwa Iye, ndipo ndisunga mau ake.


ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo chiyambire dziko lapansi.


Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;


Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.


Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa