Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 6:28 - Buku Lopatulika

28 Pamenepo anati kwa Iye, Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Pamenepo anati kwa Iye, Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Pamenepo anthu aja adayamba kufunsana kuti, “Titanitu tsono kuti titsate bwino zimene Mulungu afuna?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Kenaka anamufunsa Iye kuti, “Kodi tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 6:28
11 Mawu Ofanana  

Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzachita.


Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, chabwino nchiti ndichichite, kuti ndikhale nao moyo wosatha?


Ndipo taonani, wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?


Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.


Yesu anayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo anamtuma.


nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke?


Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?


komatu, uka, nulowe m'mzinda, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita.


Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzichita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa