Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 21:19 - Buku Lopatulika

19 Koma ichi ananena ndi kuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m'mene ananena ichi, anati kwa iye, Nditsate Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Koma ichi ananena ndi kuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m'mene ananena ichi, anati kwa iye, Nditsate Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 (Yesu adanena zimenezi pofuna kuŵadziŵitsa za m'mene Petro adzafere ndi kulemekeza Mulungu.) Atatero, adauza Petro kuti, “Unditsate.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Yesu ananena izi kumuzindikiritsa mtundu wa imfa imene Petro adzalemekezera nayo Mulungu. Kenaka Iye anati kwa Petro, “Nditsate Ine!”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 21:19
17 Mawu Ofanana  

koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo.


Ndipo iye amene satenga mtanda wake, natsata pambuyo panga, sayenera Ine.


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao.


Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.


Koma ananena ichi ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.


kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene akuti adzafa nayo.


Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m'chuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.


Yesu ananena naye, Ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza Ine, kuli chiyani ndi iwe? Unditsate Ine iwe.


monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.


podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza.


Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Musaope; munachitadi choipa ichi chonse, koma musaleka kutsata Yehova, koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa