Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 20:25 - Buku Lopatulika

25 Chifukwa chake ophunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m'chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa kunthiti yake; sindidzakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Chifukwa chake ophunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m'chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa kunthiti yake; sindidzakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “Ife taŵaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “Ndikapanda kuwona mabala a misomali m'manja mwao, ndi kupisa chala changa m'mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m'nthiti mwao, sindingakhulupirire konse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Ophunzira enawo atamuwuza Tomasi kuti iwo anaona Ambuye, iye ananenetsa kuti, “Pokhapokha nditaona zizindikiro za misomali mʼmanja ake ndi kuyikamo chala changa mʼmene munali misomali ndi kukhudza dzanja langa mʼnthiti mwake, ine sindidzakhulupirira.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 20:25
25 Mawu Ofanana  

Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye, koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.


Pakuti andizinga agalu, msonkhano wa oipa wanditsekereza; andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.


Chingakhale ichi chonse anachimwanso, osavomereza zodabwitsa zake.


Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye mfumu ya Aisraele; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye.


Ndipo iwowo, pamene anamva kuti ali moyo, ndi kuti adapenyeka kwa iye, sanamvere.


Ndipo iwowa anachoka nawauza otsala; koma iwo omwe sanawavomereze.


Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereze iwo amene adamuona, atauka Iye.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!


Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu).


Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira.


Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadziveka malaya a pathupi, pakuti anali wamaliseche, nadziponya yekha m'nyanja.


Chifukwa chake anati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Muchita chiyani?


Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


Ndipo adawalumbirira ayani kuti asalowe mpumulo wake?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa