Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:39 - Buku Lopatulika

39 Koma anadzanso Nikodemo, amene anadza kwa Iye usiku poyamba paja, alikutenga chisakanizo cha mure ndi aloe, monga miyeso zana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Koma anadzanso Nikodemo, amene anadza kwa Iye usiku poyamba paja, alikutenga chisanganizo cha mure ndi aloe, monga miyeso zana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Kudabweranso Nikodemo, yemwe uja amene adaabwera kwa Yesu usiku poyamba paja. Iye adabwera ndi mafuta onunkhira a mure osanganiza ndi aloe, kulemera kwake ngati makilogaramu 32.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Nekodimo, munthu amene poyamba pake anabwera kwa Yesu usiku, anatenga mafuta osakaniza ndi mure ndi aloe wolemera pafupifupi makilogalamu 32.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:39
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing'anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israele.


Ndipo anamuika m'manda ake adadzisemerawo m'mzinda wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osakaniza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.


Zovala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasiya; m'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani.


ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira a mure ndi chisiyo ndi sinamoni.


Wokondedwa wanga mnyamatayo ali kwa ine ngati thumba la mure, logona pakati pa mawere anga.


Narido ndi chikasu, nzimbe ndi sinamoni, ndi mitengo yonse ya lubani; mure ndi khonje, ndi zonunkhiritsa zonse zomveka.


Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, ndikamuka kuphiri la mure, ndi kuchitunda cha lubani.


bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.


Koma ambiri oyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.


Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.


Ndipo litapita Sabata, Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.


Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo.


Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anachisungira ichi tsiku la kuikidwa kwanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa