Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:31 - Buku Lopatulika

31 Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikulu, anapempha Pilato kuti miyendo yao ithyoledwe, ndipo achotsedwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikulu, anapempha Pilato kuti miyendo yao ithyoledwe, ndipo achotsedwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Paska. Akulu a Ayuda sadafune kuti mitemboyo ikhalebe pa mtanda pa tsiku la Sabata, chifukwa Lasabata limenelo linali lalikulu. Nchifukwa chake adakapempha Pilato kuti alamule kuti akathyole miyendo ya anthu opachikidwa aja, nkuŵachotsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Popeza linali Tsiku Lokonzekera ndipo tsiku linalo linali Sabata lapadera; Ayuda sanafune kuti mitembo ikhale pa mtanda pa Sabata, iwo anapempha Pilato kuti akathyole miyendo ndi kutsitsa mitemboyo.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:31
12 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.


Wolungama asamalira moyo wa choweta chake; koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.


inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.


Ndipo m'mawa mwake, ndilo tsiku lotsatana ndi tsiku lokonzera, ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhana kwa Pilato,


Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzekera, ndilo la pambuyo pa Sabata,


Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula.


Koma linali tsiku lokonza Paska; panali monga ora lachisanu ndi chimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, mfumu yanu!


Pomwepo ndipo anaika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.


Ndipo mfumu ya ku Ai, anampachika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wake pamtengo; ndipo anauponya polowera pa chipata cha mzinda; naunjikako mulu waukulu wamiyala, mpaka lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa