Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:29 - Buku Lopatulika

29 Kunaikidwako chotengera chodzala ndi vinyo wosasayo pa phesi la hisope, nachifikitsa kukamwa kwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Kunaikidwako chotengera chodzala ndi vinyo wosasayo pa phesi la hisope, nachifikitsa kukamwa kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Pomwepo panali mbiya yodzaza ndi vinyo wosasa. Asilikali aja adaviika chinkhupule m'vinyo wosasayo, nkuchitsomeka ku kamtengo ka hisope, nachifikitsa pakamwa pake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Pomwepo panali mtsuko wodzaza ndi vinyo wosasa, choncho iwo ananyika chinkhupule ndi kuchisomeka ku mtengo wa hisope nachifikitsa kukamwa kwa Yesu.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:29
9 Mawu Ofanana  

Nakamba za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebanoni kufikira hisope wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwawa pansi ndi za nsomba.


Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.


Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuuviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m'mawa.


ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.


anamwetsa Iye vinyo wosakaniza ndi ndulu; ndipo Iye, m'mene analawa, sanafune kumwa.


Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, natenga chinkhupule, nachidzaza ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye.


Ndipo Yesu, pamene anafuula ndi mau aakulu, anapereka mzimu wake.


Ndipo anathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye, nanena, Lekani; tione ngati Eliya adza kudzamtsitsa.


Ndipo asilikalinso anamnyoza, nadza kwa Iye, nampatsa vinyo wosasa,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa