Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:27 - Buku Lopatulika

27 Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Adauzanso wophunzirayo kuti, “Naŵa amai ako.” Ndipo kuyambira pamenepo wophunzirayo adaŵatenga amaiwo kumakaŵasamala kwao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Anawuzanso wophunzirayo kuti, “Nawa amayi ako.” Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzirayo anatenga amayiwo kupita nawo kwawo.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:27
11 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lake lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Ejipito.


Ndipo Yosefe anachereza atate wake ndi abale ake, ndi mbumba yonse ya atate wake ndi chakudya monga mwa mabanja ao.


Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.


Ndipo anawaunguzaunguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga.


Ndipo Petro anati, Taonani ife tasiya zathu za ife eni, ndipo takutsatani Inu.


Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire Iye.


Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,


ndi kulawirana; ndipo tinalowa m'ngalawa, koma iwo anabwera kwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa