Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mzindawo; ndipo linalembedwa mu Chihebri, ndi mu Chilatini, ndi mu Chigriki.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mudziwo; ndipo linalembedwa m'Chihebri, ndi m'Chilatini, ndi m'Chigriki.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Ayuda ambiri adachiŵerenga chidziŵitsocho, chifukwa pamalo pamene Yesu adaapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Chidziŵitsocho chidalembedwa m'chilankhulo cha Ayuda, cha Aroma, ndiponso cha Agriki.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Ayuda ambiri anawerenga chikwangwanichi, pakuti pamalo pamene Yesu anapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda ndipo chikwangwanicho chinalembedwa mu Chiaramaiki, Chilatini ndi Chigriki.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:20
11 Mawu Ofanana  

Ndipo kunalinso lembo pamwamba pake, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YA AYUDA.


Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lake, Bwalo lamiyala, koma mu Chihebri, Gabata.


Pomwepo ndipo anaika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.


Koma pali thamanda mu Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa mu Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu.


Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkulu, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Chigriki?


Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena:


Ndipo pakumva kuti analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, anaposa kukhala chete; ndipo anati,


Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? Nkukuvuta kutsalima pachotwikira.


Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata.


Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa mu Chihebri Armagedoni.


Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake mu Chihebri Abadoni, ndi mu Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa