Yohane 18:37 - Buku Lopatulika37 Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201437 Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa37 Pilato adati, “Tsono ndiye kuti ndiwedi mfumu, ati?” Yesu adati, “Mwanena nokha kuti ndine mfumu. Ine ndidabwera pansi pano ndipo ndidabadwa kuti ndidzachitire umboni choona. Aliyense wokonda choona amamva mau anga.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero37 Pilato anati, “Kani ndiwe mfumu!” Yesu anayankha kuti, “Inu mwalondola ponena kuti, Ine ndine mfumu. Kunena zoona, Ine ndinabadwa chifukwa cha chimenechi, ndipo nʼchifukwa chake ndinabwera mʼdziko lapansi, kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali mbali yachoonadi amamvera mawu anga.” Onani mutuwo |